15 Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu+ wa Eliya uli pa Elisa.” Chotero anapita kukakumana naye n’kugwada+ pamaso pake mpaka nkhope zawo pansi.
17 ‘“Ndipo m’masiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga+ pa anthu osiyanasiyana, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera. Anyamata anu adzaona masomphenya, ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+