10 Chotero Sauli ndi mtumiki wake ananyamuka kupita kuphiri kuja, ndipo kumeneko anakumana ndi kagulu ka aneneri. Nthawi yomweyo, mzimu wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye,+ moti anayamba kulankhula ngati mneneri+ pakati pa aneneriwo.
23 Pamenepo anapitiriza ulendo wake wopita ku Nayoti, ku Rama, ndipo mzimu+ wa Mulungu unafika ngakhalenso pa iye. Zitatero, iye anapitiriza kuyenda ndi kuchita zinthu ngati mneneri mpaka kukafika ku Nayoti, ku Rama.