Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 14:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndiyeno mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye,+ moti anakhadzula mkangowo pakati ngati mmene munthu angakhadzulire kamwana ka mbuzi. Iye analibe chida chilichonse m’manja mwake. Zimene anachitazi sanauze bambo kapena mayi ake.

  • 1 Samueli 11:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Sauli atamva mawu amenewa mzimu+ wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo anapsa mtima kwambiri.+

  • 1 Samueli 16:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+

  • Zekariya 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo,+ kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa makamu.

  • 2 Akorinto 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Sitinganene kuti ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha mphamvu zathu,+ koma ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha Mulungu,+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena