Numeri 11:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ine nditsikira kumeneko+ kudzalankhula nawe.+ Ndidzatengako gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe n’kuuika pa iwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyang’anira anthuwo, kuti usausenze wekhawekha.+ Oweruza 3:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Mzimu+ wa Yehova unakhala pa iye, ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Siriya m’manja mwake, moti anam’gonjetsa.+ 1 Samueli 10:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Pamenepo mzimu+ wa Yehova uyamba kugwira ntchito pa iwe, moti iweyo uyamba kulankhula monga mneneri+ pamodzi ndi aneneriwo, ndiponso usinthika kukhala wina. 2 Samueli 23:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa,+Ndipo mawu ake anali palilime langa.+
17 Ine nditsikira kumeneko+ kudzalankhula nawe.+ Ndidzatengako gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe n’kuuika pa iwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyang’anira anthuwo, kuti usausenze wekhawekha.+
10 Mzimu+ wa Yehova unakhala pa iye, ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Siriya m’manja mwake, moti anam’gonjetsa.+
6 Pamenepo mzimu+ wa Yehova uyamba kugwira ntchito pa iwe, moti iweyo uyamba kulankhula monga mneneri+ pamodzi ndi aneneriwo, ndiponso usinthika kukhala wina.