Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 11:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ine nditsikira kumeneko+ kudzalankhula nawe.+ Ndidzatengako gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe n’kuuika pa iwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyang’anira anthuwo, kuti usausenze wekhawekha.+

  • Oweruza 6:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Zitatero, Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova,+ moti anayamba kuliza lipenga+ la nyanga ya nkhosa ndipo Aabi-ezeri+ anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira.

  • Oweruza 11:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Tsopano mzimu wa Yehova unabwera pa Yefita+ ndipo anadutsa m’dera la Giliyadi, m’dera la Manase, ndi m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi.+ Atadutsa m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi anafika kwa ana a Amoni.

  • Oweruza 14:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndiyeno mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye,+ moti anakhadzula mkangowo pakati ngati mmene munthu angakhadzulire kamwana ka mbuzi. Iye analibe chida chilichonse m’manja mwake. Zimene anachitazi sanauze bambo kapena mayi ake.

  • Oweruza 15:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Choncho iye anafika ku Lehi, ndipo Afilisiti atamuona anafuula mokondwera.+ Pamenepo, mzimu wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo zingwe zimene anam’manga nazo manja zija zinaduka ngati ulusi wowauka ndi moto,+ moti zinadukaduka ndi kugwa.

  • 1 Samueli 11:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Sauli atamva mawu amenewa mzimu+ wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo anapsa mtima kwambiri.+

  • 1 Samueli 16:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+

  • 2 Mbiri 15:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Tsopano mzimu+ wa Mulungu unafikira Azariya mwana wa Odedi.+

  • Yesaya 63:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Iwo anayamba kukumbukira masiku akale, masiku a Mose mtumiki wake, ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa m’nyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake uja, ali kuti?+ Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena