29 Tsopano mzimu wa Yehova unabwera pa Yefita+ ndipo anadutsa m’dera la Giliyadi, m’dera la Manase, ndi m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi.+ Atadutsa m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi anafika kwa ana a Amoni.
14 Choncho iye anafika ku Lehi, ndipo Afilisiti atamuona anafuula mokondwera.+ Pamenepo, mzimu wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo zingwe zimene anam’manga nazo manja zija zinaduka ngati ulusi wowauka ndi moto,+ moti zinadukaduka ndi kugwa.