-
Nehemiya 9:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 “Inu ndinu Yehova, inu nokha.+ Ndinu amene munapanga kumwamba,+ ngakhale kumwambamwamba ndi makamu ake onse.+ Ndinu amene munapanga dziko lapansi+ ndi zonse zili momwemo+ komanso nyanja+ ndi zonse zili momwemo.+ Ndinu amene mukusunga zinthu zonse kuti zikhale ndi moyo. Ndipo makamu+ akumwamba amakugwadirani.
-
-
Salimo 146:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+
Nyanja ndi zonse zili mmenemo.+
Wosunga choonadi mpaka kalekale.+
-
Machitidwe 14:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 kuti: “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu+ okhala ndi zofooka+ ngati inu nomwe, ndipo tikulengeza uthenga wabwino kwa inu. Tikuchita izi kuti musiye zachabechabe zimenezi+ ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo,+ amene anapanga kumwamba,+ dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.
-
-
-