16 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola ndodo mu Yerusalemu. Ndidzathyola ndodo zimene amakolowekapo mikate yozungulira yoboola pakati.+ Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo adzachidya ali ndi nkhawa.+ Iwo adzamwa madzi ochita kuyeza ali ndi mantha,+