22 Ndidzafafaniza zolakwa zako ngati kuti ndaziphimba ndi mtambo,+ ndi machimo ako ngati kuti ndawaphimba ndi mitambo yambiri. Bwerera kwa ine,+ ndipo ine ndikuwombola.+
11 Chotero, owomboledwa a Yehova adzabwerera ku Ziyoni ndi mfuu yachisangalalo,+ ndipo pamutu pawo padzakhala chisangalalo mpaka kalekale.+ Iwo adzapeza chisangalalo ndi chimwemwe.+ Chisoni ndi kuusa moyo zidzachoka.+