Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 51:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+

      Malinga ndi kuchuluka kwa chifundo chanu, fafanizani zolakwa zanga.+

  • Salimo 103:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo,+

      Momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.+

  • Yesaya 1:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova akuti, “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+ Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.+ Ngakhale atakhala ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje.

  • Yesaya 43:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Ineyo ndi amene ndikufafaniza+ zolakwa zako,+ ndipo machimo ako sindidzawakumbukiranso.+

  • Yeremiya 33:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndiwayeretsa ku zolakwa zawo zonse zimene anachimwa nazo pamaso panga,+ ndipo ndiwakhululukira zolakwa zawo zonse zimene anandichimwira nazo ndi kuphwanya nazo malamulo anga.+

  • Machitidwe 3:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Chotero lapani+ ndi kutembenuka+ kuti machimo anu afafanizidwe,+ ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa+ zibwere kuchokera kwa Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena