Genesis 38:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa m’bale wako ndipo uchite chokolo, kuti um’berekere ana m’bale wako.”+ Deuteronomo 25:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 “Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi n’kumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mlendo wochokera m’banja lina. Mlamu wake apite kwa iye ndi kum’tenga kukhala mkazi wake, ndipo achite ukwati wa pachilamu.+ Rute 1:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Koma Naomi anati: “Bwererani ana anga. Palibe chifukwa choti tipitire limodzi. Kodi ndingathenso kubereka ana, ndipo kodi anawo angadzakhale amuna anu?+ Rute 3:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Gona pompano lero. Ngati iye angakuwombole+ mawa, zili bwino! Akuwombole. Koma ngati sakufuna kukuwombola, ineyo ndidzakuwombola. Ndithudi, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ndidzakuwombola. Gona kufikira m’mawa.” Maliko 12:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati munthu wamwalira ndi kusiya mkazi koma osasiya mwana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.+
8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa m’bale wako ndipo uchite chokolo, kuti um’berekere ana m’bale wako.”+
5 “Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi n’kumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mlendo wochokera m’banja lina. Mlamu wake apite kwa iye ndi kum’tenga kukhala mkazi wake, ndipo achite ukwati wa pachilamu.+
11 Koma Naomi anati: “Bwererani ana anga. Palibe chifukwa choti tipitire limodzi. Kodi ndingathenso kubereka ana, ndipo kodi anawo angadzakhale amuna anu?+
13 Gona pompano lero. Ngati iye angakuwombole+ mawa, zili bwino! Akuwombole. Koma ngati sakufuna kukuwombola, ineyo ndidzakuwombola. Ndithudi, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ndidzakuwombola. Gona kufikira m’mawa.”
19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati munthu wamwalira ndi kusiya mkazi koma osasiya mwana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.+