14 Iye akhale ngati malo opatulika.+ Koma kwa nyumba zonse ziwiri za Isiraeli, iye akhale ngati mwala wopunthwitsa ndiponso ngati mwala wokhumudwitsa.+ Akhalenso ngati msampha ndi khwekhwe kwa anthu okhala mu Yerusalemu.+
3 Kodi iyeyu si mmisiri wamatabwa,+ mwana wa Mariya,+ komanso m’bale wake wa Yakobo,+ Yosefe, Yudasi ndi Simoni?+ Ndipo alongo ake si awa omwe tili nawo pompano?” Choncho anayamba kukhumudwa naye.+