22 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ m’bale wake wapalamula mlandu+ wa kukhoti. Komano aliyense wonenera m’bale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe!’ adzapita ku Gehena* wamoto.+
47 Ngati diso lako limakuchimwitsa, ulitaye.+ Ndi bwino kuti ulowe mu ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana n’kuponyedwa mu Gehena uli ndi maso onse awiri,+