Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 53:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Koma zinamukomera Yehova kuti mtumiki wake aphwanyidwe.+ Iye anamulola kuti adwale.+ Mukapereka moyo wake monga nsembe ya kupalamula,+ iye adzaona ana ake.+ Adzatalikitsa masiku ake+ ndipo ndi dzanja lake, adzakwaniritsa zokonda+ Yehova.+

  • Danieli 9:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 “Pali milungu 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako+ ndi mzinda wanu woyera,+ ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo,+ athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo+ pa masomphenya ndi maulosi, ndiponso kuti adzoze Malo Opatulikitsa.+

  • 2 Akorinto 5:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Amene analibe uchimoyo,+ Mulungu anamupanga kukhala uchimo+ chifukwa cha ife, kuti tikhale olungama pamaso pa Mulungu+ kudzera mwa iye.

  • Agalatiya 3:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Khristu anatigula+ ndi kutimasula+ ku temberero la Chilamulo ndipo iyeyo anakhala temberero+ m’malo mwa ife, chifukwa Malemba amati: “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.”+

  • Tito 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Iyeyo anadzipereka+ m’malo mwa ife kuti atilanditse+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse,+ kuti tikhale anthu akeake,+ odzipereka pa ntchito zabwino.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena