Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 44:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti ndidzapatsa madzi munthu waludzu,+ ndipo ndidzaika timitsinje tamadzi pamalo ouma.+ Ndidzatsanulira mzimu wanga pambewu yako+ ndi madalitso anga pa mbadwa zako.

  • Yoweli 2:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “Zimenezi zikadzachitika ndidzatsanulira mzimu wanga+ pa chamoyo chilichonse,+ ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi+ adzanenera. Amuna achikulire adzalota maloto ndipo anyamata adzaona masomphenya.

  • Luka 3:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yohane anawayankha onsewo kuti: “Inetu ndikukubatizani m’madzi. Koma wina wamphamvu kuposa ine akubwera, amene ine sindili woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.+ Iyeyu adzakubatizani ndi mzimu woyera ndi moto.+

  • Machitidwe 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana,+ monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.

  • Machitidwe 11:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Zitatero ndinakumbukira mawu a Ambuye aja akuti, ‘Yohane anabatiza ndi madzi,+ koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.’+

  • 1 Akorinto 12:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pakuti ndi mzimu umodzi, tonsefe tinabatizidwa+ kukhala thupi limodzi, kaya tikhale Ayuda kapena Agiriki, akapolo kapena mfulu, ndipo tonsefe tinamwetsedwa+ mzimu umodzi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena