8Mosakhalitsa, Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira+ ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi.
38 Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, kuti Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye,+ anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.+