16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.
52 Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Inde, iwo anapha+ amene analengezeratu za kubwera kwa Wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndi kumupha,+