16 Pakuti sindichita nawo manyazi+ uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndi mphamvu+ ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro,+ choyamba kwa Myuda+ kenako kwa Mgiriki.+
8 Chotero, usachite manyazi ndi ntchito yochitira umboni za Ambuye wathu,+ kapena za ineyo amene ndine mkaidi chifukwa cha iye.+ Khala wokonzeka kumva zowawa+ mu mphamvu ya Mulungu+ chifukwa cha uthenga wabwino.