34 Ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene anafa, zoonadi, amenetu anaukitsidwa kwa akufa. Iye ali kudzanja lamanja+ la Mulungu, ndipo amatilankhulira mochonderera kwa Mulunguyo.+
24 Pakuti Khristu sanalowe m’malo oyera amkatikati opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Tsopano ali kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.+
2Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo.+ Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi+ wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.+