2 Mbiri 19:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Tsopano Yehu+ mwana wa Haneni+ wamasomphenya,+ anapita kukaonekera kwa Mfumu Yehosafati ndipo anaifunsa kuti: “Kodi chithandizo chiyenera kuperekedwa+ kwa oipa, ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana+ ndi Yehova?+ Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani.+ Yohane 15:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake.+ Koma popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+ Yohane 17:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Iwo ndawapatsa mawu anu, koma dziko likudana nawo,+ chifukwa sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.+ 1 Yohane 5:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu,+ koma dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.+
2 Tsopano Yehu+ mwana wa Haneni+ wamasomphenya,+ anapita kukaonekera kwa Mfumu Yehosafati ndipo anaifunsa kuti: “Kodi chithandizo chiyenera kuperekedwa+ kwa oipa, ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana+ ndi Yehova?+ Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani.+
19 Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake.+ Koma popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+
14 Iwo ndawapatsa mawu anu, koma dziko likudana nawo,+ chifukwa sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.+