2 Mbiri 32:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Koma Hezekiya sanabwezere zabwino zimene anachitiridwa,+ pakuti mtima wake unayamba kudzikuza+ ndipo mkwiyo wa Mulungu+ unayakira iyeyo, Yuda, ndi Yerusalemu. Salimo 90:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pakuti ife tatha chifukwa cha mkwiyo wanu,+Ndipo tasokonezeka chifukwa cha kupsa mtima kwanu.+ Salimo 141:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha,+Ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga,+Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+Pakuti ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.+
25 Koma Hezekiya sanabwezere zabwino zimene anachitiridwa,+ pakuti mtima wake unayamba kudzikuza+ ndipo mkwiyo wa Mulungu+ unayakira iyeyo, Yuda, ndi Yerusalemu.
5 Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha,+Ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga,+Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+Pakuti ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.+