Genesis 49:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+ Salimo 21:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Munaidalitsa ndi kuipatsa zinthu zabwino,+Ndipo pamutu pake munaika chisoti chachifumu chagolide woyengeka bwino.+ Ezekieli 21:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.*+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+ Danieli 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+ Chivumbulutso 14:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Nditayang’ana, ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panakhala winawake ngati mwana wa munthu,+ atavala chisoti chachifumu chagolide+ kumutu kwake, chikwakwa chakuthwa chili m’dzanja lake.
10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+
3 Munaidalitsa ndi kuipatsa zinthu zabwino,+Ndipo pamutu pake munaika chisoti chachifumu chagolide woyengeka bwino.+
27 Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.*+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+
14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+
14 Nditayang’ana, ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panakhala winawake ngati mwana wa munthu,+ atavala chisoti chachifumu chagolide+ kumutu kwake, chikwakwa chakuthwa chili m’dzanja lake.