Hoseya 12:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ndinalankhula ndi aneneri+ ndipo ndinawaonetsa masomphenya ochuluka. Kudzera mwa aneneri, ndinali kupereka mafanizo ambiri.+ Amosi 3:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+ Mateyu 2:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritsidwe mawu onenedwa kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”+ Machitidwe 3:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Koma mwanjira imeneyi Mulungu wakwaniritsa zimene analengezeratu kudzera mwa aneneri onse, kuti Khristu wake adzavutika.+ Aroma 1:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Uthenga umenewu anaulonjeza kalekale kudzera mwa aneneri+ ake m’Malemba oyera. Aheberi 1:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 1 Kalekale, Mulungu analankhula ndi makolo athu nthawi zambiri+ ndiponso m’njira zambiri kudzera mwa aneneri.+ Yakobo 5:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Abale, pa nkhani ya kumva zowawa+ ndi kuleza mtima,+ tengerani chitsanzo+ kwa aneneri+ amene analankhula m’dzina la Yehova.+ 1 Petulo 1:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Aneneri amene analosera+ za kukoma mtima kwakukulu kumene munali kudzasonyezedwa,+ anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndi mosamala.+
10 Ndinalankhula ndi aneneri+ ndipo ndinawaonetsa masomphenya ochuluka. Kudzera mwa aneneri, ndinali kupereka mafanizo ambiri.+
7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+
23 Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritsidwe mawu onenedwa kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”+
18 Koma mwanjira imeneyi Mulungu wakwaniritsa zimene analengezeratu kudzera mwa aneneri onse, kuti Khristu wake adzavutika.+
1 Kalekale, Mulungu analankhula ndi makolo athu nthawi zambiri+ ndiponso m’njira zambiri kudzera mwa aneneri.+
10 Abale, pa nkhani ya kumva zowawa+ ndi kuleza mtima,+ tengerani chitsanzo+ kwa aneneri+ amene analankhula m’dzina la Yehova.+
10 Aneneri amene analosera+ za kukoma mtima kwakukulu kumene munali kudzasonyezedwa,+ anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndi mosamala.+