Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse,+ popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. Choncho ndiwawonongera limodzi ndi dziko lapansi.+

  • Genesis 18:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kenako Yehova anati: “Kodi ndingamubisire Abulahamu zimene ndikufuna kuchita?+

  • 1 Mafumu 22:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Choncho Yehova waika mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri anu onsewa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”+

  • 2 Mafumu 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 chifukwa Yehova wanena kuti: “Anthu inu simuona mphepo kapena mvula, koma chigwa chonsechi chidzaza madzi.+ Inu pamodzi ndi ziweto zanu, ndithu mumwa madziwo.”’+

  • 2 Mafumu 22:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “N’chifukwa chake ndidzakugoneka+ pamodzi ndi makolo ako, ndipo ndithu udzaikidwa m’manda ako mu mtendere.+ Maso ako sadzaona tsoka lonse limene ndikulibweretsa pamalo ano.”’” Choncho iwo anabweretsa mawuwo kwa mfumuyo.

  • Salimo 25:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa,+

      Pangano lakenso ndi la anthu oterowo, ndipo iye amawadziwitsa panganolo.+

  • Yesaya 42:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Zinthu zoyamba zachitika,+ koma ndikukuuzani zinthu zatsopano. Zisanayambe kuonekera, ndimakuuzani.”+

  • Danieli 9:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Iye anandithandiza kuti ndimvetse pondiuza kuti:

      “Iwe Danieli, tsopano ndabwera kuti ndikuthandize kumvetsa zinthu zonsezi.+

  • Danieli 11:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Tsopano ndikufotokozera choonadi:+

      “Mu ufumu wa Perisiya+ mudzauka mafumu atatu, ndipo mfumu yachinayi+ idzasonkhanitsa chuma chambiri kuposa ena onsewa.+ Ndipo ikadzangokhala yamphamvu chifukwa cha chuma chakecho idzaukira ufumu wa Girisi ndi mphamvu zake zonse.+

  • Yohane 15:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Sindikutchanso inu kuti akapolo, chifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake amachita. Koma ndakutchani mabwenzi,+ chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.+

  • Chivumbulutso 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Chivumbulutso+ choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa,+ kuti aonetse akapolo ake+ zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.+ Yesuyo anatumiza mngelo wake+ kuti adzapereke Chivumbulutsocho mwa zizindikiro+ kwa kapolo wake Yohane.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena