8 Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.+ Pamenepo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”+
9 Ine Yohane, m’bale wanu ndi wogawana nanu masautso+ a Yesu,+ mu ufumu+ ndi m’kupirira,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.+