2 Chifukwa panamangidwa chipinda choyamba cha chihema ndipo mʼchipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo ndi mikate yoonetsa kwa Mulungu,+ ndipo chinkatchedwa “Malo Oyera.”+ 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+