-
Ekisodo 29:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Nkhosayo uiphe nʼkutenga magazi ake ndipo uwawaze mbali zonse za guwa lansembelo.+ 17 Nkhosayo uidule ziwaloziwalo. Kenako utsuke matumbo+ ndi ziboda zake nʼkuika chiwalo chilichonse pamodzi ndi chinzake, kuyambira kumiyendo mpaka kumutu. 18 Nkhosa yonseyo uiwotche kuti utsi wake ukwere mʼmwamba kuchokera paguwalo. Imeneyo ndi nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova, yakafungo kosangalatsa.*+ Ndi nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
-
-
Levitiko 8:18-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kenako anatenga nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+ 19 Ndiyeno Mose anapha nkhosayo nʼkuwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 20 Anaduladula nkhosayo ndipo Mose anatenga mutu wake, nyama yoduladulayo ndi mafuta ake,* nʼkuziwotcha. 21 Anatsuka matumbo ndi ziboda ndipo Mose anawotcha paguwa lansembe nkhosa yonseyo. Inali nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa.* Komanso inali nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
-
-
Levitiko 9:12-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiyeno Aroni anapha nyama ya nsembe yopsereza ndipo ana ake anamupatsa magazi a nyamayo. Atatero iye anawaza magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.+ 13 Kenako anamʼpatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza pamodzi ndi mutu ndipo anaziwotcha paguwa lansembe. 14 Atatero anatsuka matumbo komanso ziboda, nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza.
-