Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 28:3-8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Uwauze kuti, ‘Nsembe yowotcha pamoto imene muzipereka kwa Yehova ndi iyi: tsiku lililonse muzipereka nsembe yopsereza ya ana a nkhosa awiri amphongo, achaka chimodzi komanso opanda chilema.+ 4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzimupereka nsembe mʼmamawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+ 5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*+ 6 Imeneyi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku imene ndinakulamulani kuphiri la Sinai. Ndinakulamulani kuti muziipereka kwa Yehova kuti ikhale nsembe yakafungo kosangalatsa,* yowotcha pamoto. 7 Muziipereka pamodzi ndi nsembe yachakumwa chokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini. Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense+ muzipereka nsembe yachakumwa. Muzithirira Yehova nsembe yachakumwa choledzeretsa mʼmalo oyera. 8 Mwana wa nkhosa wamphongo winayo muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.* Muzimupereka limodzi ndi nsembe yambewu ndiponso yachakumwa, mofanana ndi nsembe ya mʼmamawa ija. Izikhala nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena