-
Salimo 60:6-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Popeza ndi woyera,* Mulungu walankhula kuti:
“Ndidzasangalala popereka Sekemu ngati cholowa,+
Ndipo ndidzayezera anthu anga malo mʼchigwa cha Sukoti.+
7 Giliyadi ndi wanga, ngati mmene zilili ndi Manase,+
Ndipo Efuraimu ndi chipewa choteteza* mutu wanga.
Yuda akuimira mphamvu zanga zolamula.+
8 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+
Edomu ndidzamuponyera nsapato zanga.+
Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+
-