-
Yoswa 13:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Gawo lawolo linaphatikizaponso mizinda ya mʼchigwa ya Beti-harana, Beti-nimira,+ Sukoti,+ Zafoni ndi dera lotsala la dziko la Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.+ Mtsinje wa Yorodano ndi umene unali malire awo kuchokera kumunsi kwa nyanja ya Kinereti,*+ kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano. 28 Dera limeneli linali cholowa cha anthu a fuko la Gadi chimene anapatsidwa motsatira mabanja awo. Iwo anapatsidwa derali limodzi ndi mizinda komanso midzi ya kumeneko.
-
-
Salimo 108:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Popeza ndi woyera,* Mulungu walankhula kuti:
“Ndidzasangalala popereka Sekemu+ ngati cholowa,
Ndipo ndidzayezera anthu anga malo mʼchigwa cha Sukoti.+
8 Giliyadi+ ndi wanga, ngati mmene zilili ndi Manase,
Ndipo Efuraimu ndi chipewa* choteteza mutu wanga.+
Yuda akuimira mphamvu zanga zolamula.+
9 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+
Edomu ndidzamuponyera nsapato zanga.+
Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+
-