Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 38:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Chifukwa zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+

      Sindingathe kuzisenza chifukwa zikulemera kwambiri ngati katundu wolemera.

  • Salimo 103:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Chifukwa iye akudziwa bwino mmene anatipangira,+

      Amakumbukira kuti ndife fumbi.+

  • Salimo 143:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 143 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+

      Mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo.

      Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu komanso chilungamo chanu.

       2 Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,

      Chifukwa palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+

  • Yesaya 55:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Munthu woipa asiye njira yake+

      Ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.

      Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+

      Abwerere kwa Mulungu wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mtima wonse.+

  • Danieli 9:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Inu Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve. Tsegulani maso anu kuti muone zimene zatichitikira komanso mmene mzinda wodziwika ndi dzina lanu wawonongekera. Ifeyo sitikukuchondererani chifukwa choti tachita zinthu zolungama ayi, koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+

  • Aroma 3:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho palibe munthu amene amaonedwa wolungama ndi Mulungu chifukwa chotsatira Chilamulo,+ popeza Chilamulo chimatithandiza kudziwa bwino uchimo.+

  • Tito 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 (osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene tinachita,+ koma chifukwa cha chifundo chake),+ anatipulumutsa potisambitsa kuti tifike ku moyo watsopano.+ Komanso anatipulumutsa potithandiza ndi mzimu woyera kuti tikhale atsopano.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena