Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 45:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Mulungu ndi mpando wako wachifumu mpaka kalekale.+

      Ndodo ya ufumu wako ndi ndodo yachilungamo.+

  • Salimo 72:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 72 Inu Mulungu, thandizani mfumu kuti iziweruza mogwirizana ndi zigamulo zanu,

      Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+

       2 Ateteze anthu anu pa mlandu wawo pogwiritsa ntchito chilungamo,

      Aweruze mwachilungamo milandu ya anthu anu onyozeka.+

  • Yesaya 9:6, 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Chifukwa kwa ife kwabadwa mwana,+

      Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,

      Ndipo ulamuliro* udzakhala paphewa pake.+

      Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wamuyaya, Kalonga Wamtendere.

       7 Ulamuliro* wake udzafika kutali

      Ndipo mtendere sudzatha,+

      Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake

      Kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimba

      Pogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+

      Kuyambira panopa mpaka kalekale.

      Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.

  • Yesaya 32:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Taonani! Mfumu+ idzalamulira mwachilungamo,+

      Ndipo akalonga adzalamuliranso mwachilungamo.

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzaike mfumu yolungama pampando wachifumu yochokera mʼbanja lachifumu la Davide.*+ Mfumuyo idzalamulira mʼdzikoli+ ndipo idzachita zinthu mwanzeru, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena