-
Yeremiya 46:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Tsopano ndilanga Amoni+ wa ku No,*+ Farao, Iguputo pamodzi ndi milungu yake+ ndi mafumu ake. Inde ndilanga Farao ndi onse amene amamukhulupirira.’+
26 ‘Ndidzapereka anthu a ku Iguputo mʼmanja mwa anthu amene akufuna moyo wawo, mʼmanja mwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo+ ndi mʼmanja mwa atumiki ake. Koma kenako anthu adzakhalanso mʼdzikolo ngati mmene zinalili kale,’ akutero Yehova.+
-