8 Koma mukadzalandira mzimu woyera, mudzakhala ndi mphamvu.+ Ndipo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero* a dziko lapansi.”+
8 Choncho usachite manyazi ndi ntchito yolalikira za Ambuye wathu,+ kapena kuchita manyazi ndi ineyo amene ndine mkaidi chifukwa cha iye. Koma khala wokonzeka kuvutika+ chifukwa cha uthenga wabwino ndipo uzidalira mphamvu ya Mulungu.+
9 Ine Yohane mʼbale wanu, amene mofanana ndi inu ndikupirira,+ ndikukumana ndi masautso+ ndipo tidzalamulira limodzi mu ufumu+ monga otsatira a Yesu,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.