Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Atesalonika 3
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la 2 Atesalonika

      • Pitirizani kupemphera (1-5)

      • Anawachenjeza kuti apewe makhalidwe osalongosoka (6-15)

      • Moni womaliza (16-18)

2 Atesalonika 3:1

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 15:30; 1At 5:25; Ahe 13:18
  • +Mac 19:20; 1At 1:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    1/15/1991, tsa. 23

2 Atesalonika 3:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 25:4
  • +Mac 28:24; Aro 10:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    5/1/2009, tsa. 8

    5/15/1998, tsa. 10

2 Atesalonika 3:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Yo 5:3
  • +Lu 21:19; Aro 5:3

2 Atesalonika 3:6

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “mwambo umene.”

  • *

    Mabaibulo ena amati, “tinawapatsa.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 5:14
  • +1Ak 11:2; 2At 2:15; 3:14

2 Atesalonika 3:7

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 4:16; 1At 1:6

2 Atesalonika 3:8

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “osalipira.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 20:34
  • +Mac 18:3; 1Ak 9:14, 15; 2Ak 11:9; 1At 2:9

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    12/2019, tsa. 5

2 Atesalonika 3:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 10:9, 10; 1Ak 9:6, 7
  • +1Ak 11:1; Afi 3:17

2 Atesalonika 3:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 4:11, 12; 1Ti 5:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/1987, tsa. 18

2 Atesalonika 3:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 5:14
  • +1Ti 5:13; 1Pe 4:15

2 Atesalonika 3:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aef 4:28

2 Atesalonika 3:14

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2At 3:6

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Gulu, ptsa. 144-145

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    11/2016, tsa. 12

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/1999, ptsa. 29-31

2 Atesalonika 3:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 5:14

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    11/2016, tsa. 12

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/1999, ptsa. 30-31

2 Atesalonika 3:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yoh 14:27

2 Atesalonika 3:17

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 16:21; Akl 4:18

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

2 Ates. 3:1Aro 15:30; 1At 5:25; Ahe 13:18
2 Ates. 3:1Mac 19:20; 1At 1:8
2 Ates. 3:2Yes 25:4
2 Ates. 3:2Mac 28:24; Aro 10:16
2 Ates. 3:51Yo 5:3
2 Ates. 3:5Lu 21:19; Aro 5:3
2 Ates. 3:61At 5:14
2 Ates. 3:61Ak 11:2; 2At 2:15; 3:14
2 Ates. 3:71Ak 4:16; 1At 1:6
2 Ates. 3:8Mac 20:34
2 Ates. 3:8Mac 18:3; 1Ak 9:14, 15; 2Ak 11:9; 1At 2:9
2 Ates. 3:9Mt 10:9, 10; 1Ak 9:6, 7
2 Ates. 3:91Ak 11:1; Afi 3:17
2 Ates. 3:101At 4:11, 12; 1Ti 5:8
2 Ates. 3:111At 5:14
2 Ates. 3:111Ti 5:13; 1Pe 4:15
2 Ates. 3:12Aef 4:28
2 Ates. 3:142At 3:6
2 Ates. 3:151At 5:14
2 Ates. 3:16Yoh 14:27
2 Ates. 3:171Ak 16:21; Akl 4:18
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Atesalonika 3:1-18

Kalata Yachiwiri Yopita kwa Atesalonika

3 Pomaliza abale, pitirizani kutipempherera+ kuti mawu a Yehova* apitirize kufalikira mofulumira+ komanso kulemekezedwa ngati mmene akuchitira pakati panu. 2 Muzitipemphereranso kuti tipulumutsidwe kwa anthu oipa kwambiri,+ chifukwa si anthu onse amene ali ndi chikhulupiriro.+ 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipayo. 4 Komanso monga otsatira a Ambuye, tili ndi chikhulupiriro mwa inu kuti mukutsatira malangizo amene tinakupatsani ndipo mupitiriza kuwatsatira. 5 Ambuye apitirize kutsogolera mitima yanu kuti muzikonda Mulungu+ komanso kuti muzipirira+ chifukwa cha Khristu.

6 Tsopano abale tikukupatsani malangizo mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti muzipewa mʼbale aliyense amene akuyenda mosalongosoka+ komanso amene akuchita zinthu zosagwirizana ndi malangizo amene* tinakupatsani.*+ 7 Ndipotu inuyo mukudziwa zimene mukuyenera kuchita potitsanzira,+ chifukwa sitinachite zinthu zosalongosoka pakati panu, 8 kapena kudya chakudya cha wina aliyense kwaulere.*+ Mʼmalomwake, tinagwira ntchito mwakhama komanso ndi mphamvu zathu zonse usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.+ 9 Sikuti tinachita zimenezi chifukwa choti tilibe ulamuliro wokupemphani kuti mutithandize,+ koma tinkafuna kuti tikupatseni chitsanzo choti muzitsanzira.+ 10 Ndipotu pamene tinali ndi inu, tinkakupatsani lamulo lakuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 11 Chifukwa tikumva kuti ena akuyenda mosalongosoka pakati panu,+ sakugwira ntchito nʼkomwe, koma akulowerera nkhani zimene sizikuwakhudza.+ 12 Anthu otero tikuwalamula ndi kuwachonderera mwa Ambuye Yesu Khristu kuti azigwira ntchito mwakhama popanda kulowerera nkhani za anthu ena ndipo azidya chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.+

13 Koma inuyo abale, musasiye kuchita zabwino. 14 Koma ngati wina sakumvera mawu athu amene ali mʼkalatayi, muikeni chizindikiro ndipo musiye kuchitira naye zinthu limodzi+ kuti achite manyazi. 15 Komabe musamuone ngati mdani, koma pitirizani kumulangiza+ monga mʼbale.

16 Tsopano Ambuye wamtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mʼnjira iliyonse.+ Ambuye akhale nanu nonsenu.

17 Landirani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa.+ Nthawi zonse ndimalemba chonchi mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembera.

18 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu nonsenu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena