2 Atesalonika
3 Pomalizira abale, pitirizani kutipempherera+ kuti mawu a Yehova*+ apitirize kufalikira mofulumira+ ndi kulemekezedwa ngati mmene akuchitira pakati panu. 2 Muzitero kutinso tilanditsidwe kwa anthu opweteka anzawo ndi oipa,+ pakuti chikhulupiriro sichikhala ndi anthu onse.+ 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.+ 4 Komanso ifeyo monga otsatira a Ambuye, tili ndi chikhulupiriro+ mwa inu kuti mukuchita zimene tinalamula ndipo mudzapitiriza kutero.+ 5 Ambuye apitirize kutsogolera mitima yanu kuti muzikonda+ Mulungu ndi kuti muzipirira+ chifukwa cha Khristu.
6 Tsopano tikukulangizani+ abale m’dzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe+ m’bale aliyense woyenda mosalongosoka+ komanso mosagwirizana ndi mwambo umene tinakupatsani.+ 7 Pakuti inuyo mukudziwa mmene muyenera kutitsanzirira.+ Sitinakhale mosalongosoka pakati panu,+ 8 kapena kudya chakudya cha wina aliyense kwaulere.+ M’malomwake, mwa ntchito yathu imene tinagwira mwakhama ndi thukuta lathu,+ tinagwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.+ 9 Sikuti tinatero chifukwa chopanda ulamuliro,+ koma kuti tikhale chitsanzo kwa inu, kuti inu mutitsanzire.+ 10 Ndiponso, pamene tinali ndi inu, tinali kukupatsani lamulo ili:+ “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 11 Pakuti tikumva kuti ena akuyenda mosalongosoka+ pakati panu, sakugwira ntchito n’komwe, koma akulowerera nkhani zimene sizikuwakhudza.+ 12 Anthu otero tikuwalamula ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu kuti, mwa kugwira ntchito mwakhama popanda kulowerera nkhani za anthu ena, adye chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.+
13 Koma inu abale, musaleke kuchita zabwino.+ 14 Koma ngati wina sakumvera mawu athu+ a m’kalatayi, muikeni chizindikiro+ ndipo lekani kuchitira naye zinthu limodzi,+ kuti achite manyazi.+ 15 Komabe musamuone monga mdani, koma pitirizani kumulangiza+ monga m’bale.
16 Tsopano Ambuye wamtendere mwiniyo, akupatseni mtendere nthawi zonse m’njira iliyonse.+ Ambuye akhale nanu nonsenu.
17 Landirani moni wanga, ineyo Paulo, wolemba ndekha m’kalembedwe kanga,+ komwe ndi chizindikiro m’kalata yanga iliyonse. Aka ndiko kalembedwe kanga.
18 Kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu nonsenu.