Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chivumbulutso 21
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Chivumbulutso

      • Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano (1-8)

        • Sikudzakhalanso imfa (4)

        • Zinthu zonse zidzakhala zatsopano (5)

      • Anafotokoza zokhudza Yerusalemu watsopano (9-27)

Chivumbulutso 21:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 65:17; 66:22; 2Pe 3:13
  • +2Pe 3:10; Chv 20:11
  • +Yes 57:20

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    11/2023, tsa. 4

    Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo, article 33

    Utumiki Komanso Moyo Wathu,

    12/2019, tsa. 6

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 301

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/2001, tsa. 31

    4/15/2000, tsa. 12

    7/15/1991, ptsa. 5-6

    9/15/1990, tsa. 6

    Galamukani!,

    1/8/1997, tsa. 31

    Kukambitsirana, ptsa. 133-134

Chivumbulutso 21:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 3:12
  • +Chv 19:7

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, ptsa. 4-5

    7/1/1995, ptsa. 13-14

    1/1/1993, tsa. 7

    7/15/1991, ptsa. 5-6

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 301-303

    Kukambitsirana, tsa. 134

    Chisungiko cha Padziko Lonse, ptsa. 92-93, 95-97

Chivumbulutso 21:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eze 37:27

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 26

    Nsanja ya Olonda,

    3/15/2013, tsa. 23

    7/15/1991, ptsa. 5-6

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 303

    Kukambitsirana, tsa. 134

    Chisungiko cha Padziko Lonse, ptsa. 177-178

    “Tawonani!,” ptsa. 29-30

Chivumbulutso 21:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 7:17
  • +Yes 25:8; 1Ak 15:26
  • +Yes 35:10; 65:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 2

    Galamukani!,

    No. 1 2021 tsa. 13

    7/8/1994, ptsa. 21-22, 27-28

    Nsanja ya Olonda,

    12/1/2013, tsa. 11

    9/15/2012, tsa. 10

    8/1/2012, tsa. 22

    1/15/2012, tsa. 30

    12/1/2009, ptsa. 5-6

    8/15/2006, tsa. 31

    4/15/2000, ptsa. 12-13

    7/15/1990, tsa. 5

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 303

    Chisungiko cha Padziko Lonse, ptsa. 177-178

    “Tawonani!,” ptsa. 29-30

Chivumbulutso 21:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 4:2, 3
  • +2Pe 3:13

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    11/2023, ptsa. 3-4

    Yandikirani, ptsa. 81-86

    Utumiki Komanso Moyo Wathu,

    12/2019, tsa. 6

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 303-304

    Nsanja ya Olonda,

    4/15/2000, tsa. 14

    7/15/1991, ptsa. 5-6

    3/1/1987, ptsa. 28-32

Chivumbulutso 21:6

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “ndine A ndi Z.” Alefa ndi chilembo choyambirira cha afabeti ya Chigiriki ndipo Omega ndi chilembo chomalizira.

  • *

    Kapena kuti, “popanda mtengo.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 1:8; 22:13
  • +Sl 36:9; Yes 55:1; Chv 7:17; 22:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    11/2023, ptsa. 3, 4-7

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    10/2016, ptsa. 21-22

    Baibulo la Dziko Latsopano (nwt), tsa. 2136

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 303-304

Chivumbulutso 21:7

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 304

Chivumbulutso 21:8

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Yo 5:10
  • +1Yo 3:15
  • +Aef 5:5
  • +Yoh 8:44
  • +Chv 19:20
  • +Miy 10:7; Ahe 10:26, 27; Chv 2:11; 20:6

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Baibulo la Dziko Latsopano (nwt), tsa. 2148

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 304-305

    Nsanja ya Olonda,

    7/1/1987, ptsa. 24-25

Chivumbulutso 21:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 15:1
  • +Chv 19:7

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Nsanja ya Olonda,

    2/15/2007, tsa. 13

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 305-306

Chivumbulutso 21:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ahe 12:22; Chv 3:12; 21:2

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 305-306

Chivumbulutso 21:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 60:1, 2
  • +Eks 24:9, 10

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 302, 305-306

Chivumbulutso 21:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 302, 306

Chivumbulutso 21:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 22:14

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 302, 306

Chivumbulutso 21:14

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 10:2-4; Lu 6:13-16; Mac 1:13

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 302, 306

    Nsanja ya Olonda,

    10/15/1997, ptsa. 13-14

Chivumbulutso 21:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eze 40:3, 5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 306

Chivumbulutso 21:16

Mawu a M'munsi

  • *

    Pafupifupi makilomita 2,220. Sitadiya imodzi ndi yofanana ndi mamita 185. Onani Zakumapeto B14.

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 306-307

Chivumbulutso 21:17

Mawu a M'munsi

  • *

    Mamita pafupifupi 64. Onani Zakumapeto B14.

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 306-307

Chivumbulutso 21:18

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 4:3; 21:10, 11

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 307-308

Chivumbulutso 21:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 307-308

Chivumbulutso 21:20

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 307-308

Chivumbulutso 21:21

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 307-308

Chivumbulutso 21:22

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 6:3

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    5/2022, ptsa. 17-18

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 308-309

Chivumbulutso 21:23

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 60:19, 20; Chv 22:5
  • +Yoh 1:9; Mac 26:13, 15; Ahe 1:3

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 308-309

Chivumbulutso 21:24

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 60:3

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 310

Chivumbulutso 21:25

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 60:11, 20

Chivumbulutso 21:26

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 60:5

Chivumbulutso 21:27

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 5:6; Yes 52:1; 1Ak 6:9, 10; Aga 5:19-21; Chv 21:8
  • +Da 12:1; Afi 4:3; Chv 13:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 306, 310

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

Chiv. 21:1Yes 65:17; 66:22; 2Pe 3:13
Chiv. 21:12Pe 3:10; Chv 20:11
Chiv. 21:1Yes 57:20
Chiv. 21:2Chv 3:12
Chiv. 21:2Chv 19:7
Chiv. 21:3Eze 37:27
Chiv. 21:4Chv 7:17
Chiv. 21:4Yes 25:8; 1Ak 15:26
Chiv. 21:4Yes 35:10; 65:19
Chiv. 21:5Chv 4:2, 3
Chiv. 21:52Pe 3:13
Chiv. 21:6Chv 1:8; 22:13
Chiv. 21:6Sl 36:9; Yes 55:1; Chv 7:17; 22:1
Chiv. 21:81Yo 5:10
Chiv. 21:81Yo 3:15
Chiv. 21:8Aef 5:5
Chiv. 21:8Yoh 8:44
Chiv. 21:8Chv 19:20
Chiv. 21:8Miy 10:7; Ahe 10:26, 27; Chv 2:11; 20:6
Chiv. 21:9Chv 15:1
Chiv. 21:9Chv 19:7
Chiv. 21:10Ahe 12:22; Chv 3:12; 21:2
Chiv. 21:11Yes 60:1, 2
Chiv. 21:11Eks 24:9, 10
Chiv. 21:13Chv 22:14
Chiv. 21:14Mt 10:2-4; Lu 6:13-16; Mac 1:13
Chiv. 21:15Eze 40:3, 5
Chiv. 21:18Chv 4:3; 21:10, 11
Chiv. 21:22Eks 6:3
Chiv. 21:23Yes 60:19, 20; Chv 22:5
Chiv. 21:23Yoh 1:9; Mac 26:13, 15; Ahe 1:3
Chiv. 21:24Yes 60:3
Chiv. 21:25Yes 60:11, 20
Chiv. 21:26Yes 60:5
Chiv. 21:27Sl 5:6; Yes 52:1; 1Ak 6:9, 10; Aga 5:19-21; Chv 21:8
Chiv. 21:27Da 12:1; Afi 4:3; Chv 13:8
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Chivumbulutso 21:1-27

Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira

21 Ndiyeno ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,+ chifukwa kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka+ ndipo kulibenso nyanja.+ 2 Ndinaonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu+ ndipo unali utakonzedwa ngati mkwatibwi amene wavala zokongola kuti akalandire mwamuna wake.+ 3 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu akuti: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu ndipo iye azidzakhala nawo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulunguyo adzakhala nawo.+ 4 Iye adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo+ ndipo imfa sidzakhalaponso.+ Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka.+ Zakalezo zapita.”

5 Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu+ anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.”+ Ananenanso kuti: “Lemba, chifukwa mawu amenewa ndi odalirika komanso oona.” 6 Iye anandiuza kuti: “Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega,* chiyambi ndi mapeto.+ Aliyense amene akumva ludzu ndidzamupatsa madzi a kasupe wa moyo kwaulere.*+ 7 Aliyense amene wapambana pankhondo adzalandira zinthu zimenezi kuti zikhale cholowa chake. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake ndipo iye adzakhala mwana wanga. 8 Koma anthu amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu,+ achiwerewere,*+ amene amachita zamizimu, olambira mafano ndi anthu onse abodza,+ adzaponyedwa mʼnyanja yoyaka moto ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+

9 Mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliri 7 yotsiriza+ anabwera nʼkundiuza kuti: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.”+ 10 Choncho, pogwiritsa ntchito mphamvu ya mzimu, ananditenga nʼkundipititsa kuphiri lalikulu ndi lalitali ndipo anandionetsa mzinda woyera wa Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu,+ 11 ndipo unali ndi ulemerero wa Mulungu.+ Unkanyezimira ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.+ 12 Mzindawo unali ndi mpanda waukulu komanso wautali ndipo unali ndi mageti 12. Pamagetiwo panali angelo 12 ndipo panalembedwa mayina a mafuko 12 a ana a Isiraeli. 13 Kumʼmawa kwa mzindawo kunali mageti atatu, kumpoto mageti atatu, kumʼmwera mageti atatu ndipo kumadzulo kwake kunali mageti atatu.+ 14 Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko yokwana 12 ndipo pamiyalayo panalembedwa mayina 12 a atumwi 12+ a Mwanawankhosa.

15 Ndiyeno amene ankandilankhula uja ananyamula bango lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, mageti ake ndi mpanda wake.+ 16 Mzindawo unali ndi mbali 4 zofanana kutalika kwake. Mulitali mwake nʼchimodzimodzi ndi mulifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawo ndi bangolo ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000* kuuzungulira. Mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso kuchoka pansi kupita mʼmwamba ndi zofanana. 17 Anayezanso mpanda wake ndipo unali wautali mikono 144,* mogwirizana ndi muyezo umene munthu anapeza, umenenso ndi wofanana ndi muyezo wa mngelo. 18 Mpandawo unamangidwa ndi mwala wa yasipi+ ndipo mzindawo unamangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. 19 Maziko a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yosiyanasiyana: maziko oyamba anali amwala wa yasipi, achiwiri wa safiro, achitatu wa kalikedo, a 4 wa emarodi, 20 a 5 wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto ndipo a 12 wa ametusito. 21 Komanso zitseko za mageti 12 aja zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinapangidwa ndi ngale imodzi. Ndipo msewu waukulu wamumzindawo unapangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi.

22 Mumzindawo sindinaonemo kachisi aliyense chifukwa kachisi wake ndi Yehova* Mulungu Wamphamvuyonse+ komanso Mwanawankhosa. 23 Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, chifukwa kuwala kwa ulemerero wa Mulungu kunkaunikira mzindawo+ ndipo Mwanawankhosa ndi amene anali nyale yake.+ 24 Kuwala kwake kudzaunikira njira ya mitundu ya anthu kuti ithe kuyenda+ ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo. 25 Mageti ake sadzatsekedwa nʼkomwe, chifukwa kudzakhala masana okha ndipo usiku sudzakhalako.+ 26 Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo.+ 27 Koma chilichonse chodetsedwa komanso aliyense wochita zonyansa ndiponso zachinyengo, sadzalowa mumzindawo.+ Amene adzalowemo ndi okhawo amene mayina awo analembedwa mumpukutu wa moyo wa Mwanawankhosa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena