21 Zochitika Zazikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi
Zochitika za m’Mauthenga Abwino Anayi, Zondandalikidwa Motsatira Nthawi Imene Zinachitika
Zochitika Zotifikitsa pa Nthawi ya Utumiki wa Yesu
NTHAWI |
MALO |
CHOCHITIKA |
LEMBA |
---|---|---|---|
3 B.C.E. |
Yerusalemu, m’kachisi |
Zekariya auzidwiratu za kubadwa kwa Yohane M’batizi |
|
c. 2 B.C.E. |
Nazareti, ku Yudeya |
Mariya auzidwiratu za kubadwa kwa Yesu, ndipo achezera Elizabeti |
|
2 B.C.E. |
Dera la kumapiri la Yudeya |
Kubadwa kwa Yohane M’batizi. Pambuyo pake, moyo wake m’chipululu |
|
2 B.C.E., c. Oct. 1 |
Betelehemu |
Kubadwa kwa Yesu (Mawuyo, amene zinthu zonse zinakhalako kudzeramwa iye) monga mbadwa ya Abulahamu ndi ya Davide |
|
Pafupi ndi Betelehemu |
Mngelo alengeza nkhani yabwino.Abusa apita kukaona mwana wakhandayo |
||
Betelehemu, Yerusalemu |
Yesu adulidwa (tsiku la 8), aperekedwa m’kachisi (tsiku la 40) |
||
1 B.C.E. kapena 1 C.E. |
Yerusalemu, Betelehemu, Nazareti |
Okhulupirira nyenyezi. Athawira ku Iguputo. Ana akhanda aphedwa. Yesu abwerera |
|
12 C.E. |
Yerusalemu |
Yesu wa zaka 12 pa chikondwerero cha Pasika. Apita kunyumba |
|
29, chakumayambiriro kwa chaka |
Chipululu, Yorodano |
Utumiki wa Yohane M’batizi |
Chiyambi cha Utumiki wa Yesu
NTHAWI |
MALO |
CHOCHITIKA |
LEMBA |
---|---|---|---|
29, chakumapeto kwa chaka |
Mtsinje wa Yorodano |
Ubatizo ndi kudzozedwa kwa Yesu, wobadwa monga munthu mu mzera wa Davide, koma wolengezedwa kukhala Mwana wa Mulungu |
|
Chipululu cha Yudeya |
Yesu asala kudya ndipo ayesedwa |
||
Betaniya wa kutsidya lina la Yorodano |
Umboni wa Yohane M’batizi wonenaza Yesu |
||
Kumtunda kwa chigwa cha Yorodano |
Ophunzira oyamba a Yesu |
||
Kana wa ku Galileya, Kaperenao |
Chozizwitsa choyamba cha Yesu. Apita ku Kaperenao |
||
30, Pasika |
Yerusalemu |
Kuchita Pasika. Athamangitsa amalonda m’kachisi |
|
Yerusalemu |
Yesu akambirana ndi Nikodemo |
||
Yudeya, Ainoni |
Ophunzira a Yesu abatiza anthu. Yohane azicheperachepera |
||
Tiberiyo |
Yohane aponyedwa m’ndende. Yesu anyamuka kupita ku Galileya |
||
Sukari, ku Samariya |
Pa ulendo wa ku Galileya, Yesu aphunzitsa Asamariya |
Utumiki Waukulu wa Yesu m’Galileya
NTHAWI |
MALO |
CHOCHITIKA |
LEMBA |
---|---|---|---|
30, Pasika |
Galileya |
Choyamba alengeza kuti, “Ufumu wakumwamba wayandikira” |
|
Nazareti, Kana, Kaperenao |
Achiritsa mnyamata, awerenga za ntchito yake, akanidwa, apita ku Kaperenao |
||
Nyanja ya Galileya, pafupi ndi Kaperenao |
Kuitanidwa kwa Simoni ndi Andireya, Yakobo ndi Yohane |
||
Kaperenao |
Achiritsa waziwanda, apongozi a Petulo, ndi enanso ambiri |
||
Galileya |
Ulendo woyamba wozungulira mu Galileya, ali ndi ophunzira anayi oitanidwa kumene |
||
Galileya |
Wakhate achiritsidwa, anthu miyandamiyanda akhamukira kwa Yesu |
||
Kaperenao |
Achiritsa wakufa ziwalo |
||
Kaperenao |
Kuitanidwa kwa Mateyu. Achita phwando ndi okhometsa msonkho |
||
Yudeya |
Alalikira m’masunagoge a ku Yudeya |
||
31, Pasika |
Yerusalemu |
Achita nawo phwando, achiritsa mwamuna wina, adzudzula Afarisi |
|
Kubwerera kuchokera ku Yerusalemu(?) |
Ophunzira abudula ngala za tirigu pa Sabata |
||
Galileya, nyanja ya Galileya |
Achiritsa dzanja pa Sabata, apita kukapumula kugombe la nyanja, achiritsa anthu |
||
Phiri la pafupi ndi Kaperenao |
Anthu 12 asankhidwa kukhala atumwi |
||
Pafupi ndi Kaperenao |
Ulaliki wa paphiri |
||
Kaperenao |
Achiritsa wantchito wa kapitawo wa asilikali |
||
Naini |
Aukitsa mwana wa mkazi wamasiye |
||
Galileya |
Yohane m’ndende atumiza ophunzira ake kwa Yesu |
||
Galileya |
Mizinda idzudzulidwa, kuululira zinthu tiana, goli lofewa |
||
Galileya |
Mzimayi wochimwa athira mafuta pamapazi ake, fanizo la anthu angongole |
||
Galileya |
Ulendo wachiwiri wolalikira m’Galileya, limodzi ndi atumwi 12 |
||
Galileya |
Waziwanda achiritsidwa, Yesu akum’neneza kuti ndi wogwirizana ndi Belezebule |
||
Galileya |
Alembi ndi Afarisi afuna kuona chizindikiro |
||
Galileya |
Ophunzira a Khristu ndiwo achibale ake enieni |
||
Nyanja ya Galileya |
Mafanizo a wofesa mbewu, namsongole, ndi ena. Mafotokozedwe ake |
||
Nyanja ya Galileya |
Podutsa nyanja aimitsa mphepo yamkuntho |
||
Gadara, Kum’mwera chakum’mawa ya nyanja ya Galileya |
Aziwanda awiri achiritsidwa, nkhumba zigwidwa ndi ziwanda |
||
Mwina ku Kaperenao |
Mwana wamkazi wa Yairo aukitsidwa, mkazi achiritsidwa |
||
Kaperenao(?) |
Achiritsa amuna awiri akhungu ndi waziwanda wosalankhula |
||
Nazareti |
Achezeranso mzinda umene anakulirako ndipo akanidwanso |
||
Galileya |
Ulendo wachitatu woyendera Galileya, madera ambiri ayenderedwa iye atatumiza atumwi |
||
Tiberiyo |
Yohane M’batizi adulidwa mutu, mantha a Herode chifukwa cha mlanduwo |
||
32, chikondwerero cha Pasika chitayandikira (Yoh 6:4) |
Kaperenao(?), Kumpoto chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya |
Atumwi abwerako pa ulendo wokalalikira, 5,000 adyetsedwa |
|
Kumpoto chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya, Genesarete |
Ayesa kulonga Yesu ufumu, ayenda panyanja, achiritsa anthu |
||
Kaperenao |
Afotokoza za “chakudya chopatsamoyo,” ophunzira ambiri asiya kum’tsatira |
||
32, pambuyo pa Pasika |
Mwina ku Kaperenao |
Miyambo yochititsa Mawu a Mulungu kukhala opanda pake |
|
Foinike, |
Pafupi ndi Turo, Sidoni. Kenako ku Dekapole, 4,000 adyetsedwa |
||
Magadani |
Asaduki ndi Afarisi afunanso chizindikiro |
||
Kumpoto chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya, Betsaida |
Achenjeza za chofufumitsa cha Afarisi, achiritsa wakhungu |
||
Kaisareya wa Filipi |
Yesu Mesiya, aneneratu za imfa yake, kuukitsidwa |
||
Mwina phiri la Herimoni |
Kusandulika pamaso pa Petulo, Yakobo, ndi Yohane |
||
Kaisareya wa Filipi |
Achiritsa waziwanda amene ophunzira alephera kum’chiritsa |
||
Galileya |
Aneneratunso za imfa yake ndi kuukitsidwa kwake |
||
Kaperenao |
Ndalama yokakhomera msonkho iperekedwa mozizwitsa |
||
Kaperenao |
Wamkulu koposa mu Ufumu. Kukambirana zolakwa, chifundo |
||
Galileya, Samariya |
Anyamuka ku Galileya apita ku Chikondwerero cha Misasa. Zonse azipatulira utumiki |
Utumiki wa Yesu Wakumapeto mu Yudeya
NTHAWI |
MALO |
CHOCHITIKA |
LEMBA |
---|---|---|---|
32, Chikondwerero cha Misasa |
Yerusalemu |
Yesu aphunzitsa anthu pa Chikondwerero cha Misasa |
|
Yerusalemu |
Kuphunzitsa pambuyo pa Chikondwererocho, achiritsa akhungu |
||
Mwina ku Yudeya |
Atumwi 70 atumizidwa kukalalikira, abwerako, apereka lipoti |
||
Yudeya, Betaniya |
Afotokoza za Msamariya wachifundo. Panyumba ya Malita, Mariya |
||
Mwina ku Yudeya |
Aphunzitsanso pemphero lachitsanzo. Kulimbikira kupempha |
||
Mwina ku Yudeya |
Akana mlandu womunamizira. Asonyeza kuti m’badwowo ndi woyenera chilango |
||
Mwina ku Yudeya |
Pa chakudya kwa Mfarisi, Yesu adzudzula achinyengo |
||
Mwina ku Yudeya |
Akamba nkhani ya mmene Mulungu Amatisamalira. Mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika |
||
Mwina ku Yudeya |
Achiritsa mkazi wolumala pa Sabata, mafanizo atatu |
||
32, Chikondwerero cha Kupereka Kachisi kwa Yesu pa Mulungu |
Yerusalemu |
Chikondwerero cha Kupereka Kachisi kwa Mulungu. M’busa Wabwino |
Utumiki wa Yesu Wakumapeto Kum’mawa kwa Yorodano
NTHAWI |
MALO |
CHOCHITIKA |
LEMBA |
---|---|---|---|
32, Chikondwerero cha Kupereka Kachisi kwa Yesu pa Mulungu |
Tsidya la Yorodano |
Ambiri akhulupirira Yesu |
|
Pereya (kutsidya la Yorodano) |
Aphunzitsa m’mizinda, m’midzi, alowera ku Yerusalemu |
||
Pereya |
Kulowa mu Ufumu, Herode aopseza, nyumba yabwinja |
||
Mwina ku Pereya |
Kudzichepetsa, fanizo la phwando lalikulu la chakudya chamadzulo |
||
Mwina ku Pereya |
Kuwerengera mtengo wa kukhala wophunzira |
||
Mwina ku Pereya |
Mafanizo: nkhosa yotayika, ndalama yotayika, mwana wolowerera |
||
Mwina ku Pereya |
Mafanizo: mtumiki woyang’anira nyumba wosalungama, munthu wolemera ndi Lazaro |
||
Mwina ku Pereya |
Kukhululukira ndi chikhulupiriro, akapolo opanda pake |
||
Betaniya |
Lazaro aukitsidwa kwa akufa ndi Yesu |
||
Yerusalemu, Efuraimu |
Uphungu wa Kayafa kuti Yesu aphedwe, Yesu achokako |
||
Samariya, Galileya |
Achiritsa ndi kuphunzitsa anthu pa ulendo wake wodutsa m’Samariya, Galileya |
||
Samariya kapena Galileya |
Mafanizo: mkazi wamasiye wolimbikira kupempha, Mfarisi ndi wokhometsa msonkho |
||
Pereya |
Adutsa m’Pereya, aphunzitsa za kuthetsa ukwati |
||
Pereya |
Alandira ndi kudalitsa ana aang’ono |
||
Pereya |
Mwamuna wachinyamata wolemera, fanizo la antchito am’munda wa mpesa |
||
Mwina ku Pereya |
Kachitatu Yesu aneneratu za imfa yake, kuukitsidwa |
||
Mwina ku Pereya |
Kupemphera malo Yakobo ndi Yohane mu Ufumu |
||
Yeriko |
Podutsa m’Yeriko achiritsa amuna awiri akhungu, achezera Zakeyu. Fanizo la ndalama 10 za mina |
Utumiki Womaliza wa Yesu m’Yerusalemu
NTHAWI |
MALO |
CHOCHITIKA |
LEMBA |
---|---|---|---|
Nisani 8, 33 |
Betaniya |
Afika ku Betaniya masiku 6 Pasika asanachitike |
|
Nisani 9 |
Betaniya |
Phwando panyumba ya Simoni wakhate, Mariya athira mafuta Yesu, Ayuda afika kudzaona Yesu ndi Lazaro |
|
Betaniya-Yerusalemu |
Khristu alowa monga wopambana m’Yerusalemu |
||
Nisani 10 |
Betaniya-Yerusalemu |
Mkuyu wosabala utembereredwa, kuyeretsa kachisi kachiwiri |
|
Yerusalemu |
Ansembe aakulu ndi alembi akonza chiwembu kuti aphe Yesu |
||
Yerusalemu |
Kukambirana ndi Agiriki, kusakhulupirira kwa Ayuda |
||
Nisani 11 |
Betaniya-Yerusalemu |
Mkuyu wosabala aupeza utauma |
|
Yerusalemu, m’kachisi |
Akayikira ulamuliro wa Khristu, fanizo la ana aamuna awiri |
||
Yerusalemu, m’kachisi |
Mafanizo a olima munda oipa, phwando la ukwati |
||
Yerusalemu, m’kachisi |
Mafunso ofuna kum’kola nawo pa nkhani za msonkho, kuuka kwa akufa, ndi lamulo |
||
Yerusalemu, m’kachisi |
Funso la Yesu lowagometsa pa nkhani ya mzera wobadwiramo wa Mesiya |
||
Yerusalemu, m’kachisi |
Adzudzula mwamphamvu alembi ndi Afarisi |
||
Yerusalemu, m’kachisi |
Kakhobidi ka mkazi wamasiye |
||
Phiri la Maolivi |
Aneneratu za kugwa kwa Yerusalemu, kukhalapo kwa Yesu, mapeto a nthawi ino |
||
Phiri la Maolivi |
Mafanizo a anamwali 10, matalente, nkhosa ndi mbuzi |
||
Nisani 12 |
Yerusalemu |
Atsogoleri achipembedzo akonza zopha Yesu |
|
Yerusalemu |
Yudasi akambirana ndi ansembe za kupereka Yesu |
||
Nisani 13 (Lachinayi masana) |
Pafupi ndi Yerusalemu, ndi mkati mwake |
Kukonzekera Pasika |
|
Nisani 14 |
Yerusalemu |
Adya chakudya cha Pasika pamodzi ndi atumwi 12 |
|
Yerusalemu |
Yesu asambitsa mapazi a atumwi ake |
||
Yerusalemu |
Yudasi aululika kuti ndiye adzam’pereke ndipo auzidwa kuchoka |
||
Yerusalemu |
Chakudya chamadzulo cha Chikumbutso chikhazikitsidwa ndi atumwi 11 |
||
Yerusalemu |
Aneneratu za kukanidwa ndi Petulo, ndi kubalalika kwa atumwi |
||
Yerusalemu |
Mthandizi, kukondana, chisautso, pemphero la Yesu |
||
Getsemane |
Kuzunzika mumtima m’mundamo, kuperekedwa ndi kumangidwa kwa Yesu |
||
Yerusalemu |
Kuzengedwa mlandu ndi Anasi, Kayafa, Khoti Lalikulu la Ayuda. Petulo am’kana |
||
Yerusalemu |
Yudasi wom’perekayo adzimangirira |
||
Yerusalemu |
Pamaso pa Pilato, kenako kwa Herode, n’kubwereranso kwa Pilato |
||
Yerusalemu |
Aperekedwa kukaphedwa, Pilato atayesa kum’masula |
||
(Cha m’ma3 koloko masana, Lachisanu) |
Gologota, Yerusalemu |
Imfa ya Yesu pamtengo wozunzikirapo, ndi zochitika zotsatira |
|
Yerusalemu |
Mtembo wa Yesu auchotsa pamtengo wozunzikirapo ndi kukauika |
||
Nisani 15 |
Yerusalemu |
Ansembe ndi Afarisi aika alonda pamanda |
|
Nisani 16 |
Yerusalemu ndi madera apafupi |
Kuuka kwa Yesu ndi zochitika za pa tsikulo |
|
Yerusalemu, Galileya |
Yesu Khristu aonekera kangapo |
||
Iyari 25 |
Phiri la Maolivi, pafupi ndi Betaniya |
Yesu akwera kumwamba, tsiku la 40 pambuyo pa kuuka kwake |