Zamkatimu
September 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
October 24-30, 2011
TSAMBA 7
October 31, 2011–November 6, 2011
Kodi Mukulola Yehova Kukhala Cholowa Chanu?
TSAMBA 11
November 7-13, 2011
Tiyeni Tithamange Mpikisano Mopirira
TSAMBA 16
November 14-20, 2011
‘Thamangani N’cholinga Choti Mukalandire Mphoto’
TSAMBA 20
November 21-27, 2011
TSAMBA 25
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA 1, 2 TSAMBA 7-15
Kodi Yehova anatanthauza chiyani pamene anauza Alevi kuti: ‘Ine ndine cholowa chako?’ (Num. 18:20) Kodi ndi Alevi okha amene anali ndi mwayi woti Yehova akhale cholowa chawo? Kodi Yehova akhoza kukhala cholowa chathu masiku ano? Ngati ndi choncho kodi zingatheke bwanji? Nkhani ziwirizi zifotokoza mmene Yehova angakhalire cholowa chathu.
NKHANI ZOPHUNZIRA 3, 4 TSAMBA 16-24
Nkhani ziwirizi zitithandiza kuona zimene tingachite kuti tithamange bwinobwino mpikisano n’kukalandira mphoto. Kodi n’chiyani chingatithandize ndiponso kutilimbikitsa pa mpikisanowu? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatisokoneze kapena kutikola zomwe tiyenera kupewa? Nanga n’chiyani chingatithandize kuti tithamange mpaka kufika pamzere womaliza?
NKHANI YOPHUNZIRA 5 TSAMBA 25-29
Yehova amadziwa ndiponso kuvomereza atumiki ake okhulupirika. Kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova? Nkhaniyi ithandiza aliyense wa ife kudzifufuza.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI:
3 Kuwerenga Baibulo Kwandilimbikitsa pa Moyo Wanga Wonse
30 Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi