MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzikhulupirira Kwambiri Mawu a Mulungu
Mawu a Mulungu akhoza kusintha moyo wathu. (Ahe 4:12) Komabe kuti malangizo komanso uphungu wake uzitithandiza, tiyenera kukhulupirira kuti ndi “mawu a Mulungu.” (1At 2:13) Kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri Baibulo?
Tsiku lililonse tiziwerenga kachigawo kenakake ka Baibulo. Tikamawerenga, tizifufuza umboni woti Yehova ndi amene analilemba. Mwachitsanzo, fufuzani malangizo anzeru omwe amapezeka m’buku la Miyambo, ndipo onani mmene amatithandiziranso ifeyo masiku ano.—Miy 13:20; 14:30.
Yambani kuphunzira zokhudza Baibulo. Muzipeza maumboni otsimikizira kuti Baibulo ndi buku louziridwa. Mu Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani, pitani pamene alemba kuti “Baibulo” kenako “Kuuziridwa ndi Mulungu.” Mungalimbitsenso chikhulupiriro chanu chakuti uthenga wa m’Baibulo sunasinthe pofufuza mfundo zimene zili mu Nsanja ya Olonda Na. 4 2016.
ONERANI VIDIYO YAKUTI N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAKHULUPIRIRA . . . MAWU A MULUNGU?, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi zomwe zinapezeka pa khoma la kachisi ku Kanaki ku Iguputo, zimatsimikizira bwanji kuti Baibulo limanena zoona?
Kodi timadziwa bwanji kuti uthenga wa m’Baibulo sunasinthe?
Kodi mfundo yakuti Baibulo lapulumuka zambiri imakutsimikizirani bwanji kuti ndi Mawudi a Mulungu?—Werengani Yesaya 40:8