Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/97 tsamba 8
  • Phunzitsani Ena Zimene Mulungu Amafuna

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunzitsani Ena Zimene Mulungu Amafuna
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Dalirani Yehova Kuti Akulitse Zinthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 4/97 tsamba 8

Phunzitsani Ena Zimene Mulungu Amafuna

1 Anthu ambiri amene amanidwa mwauzimu “kumva mawu a Yehova” amapezekabe. (Amosi 8:11) Pamene kuli kwakuti ena amakhulupirira kuti Mulungu aliko, iwo samadziŵa chifuno chake ndi zimene amafuna. Choncho, ifeyo tifunikiradi kuwaphunzitsa choonadi cha Ufumu chopulumutsa moyo. Mwa kukhala ndi ziŵiya zoyenera ndi kukhala okonzekera kulalikira nthaŵi iliyonse, tingapeze awo amene akufuna kuphunzira zimene Yehova amafuna.

2 Mu April ndi May, tidzakhala ndi makope ogaŵira apanthaŵi yake a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndiponso, kwa nthaŵi yoyamba, tidzagaŵira brosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Zithunzi zake zokopa ndi mafunso ake ochititsa munthu kuganiza zimachititsa broshali kukopa anthu ambiri. Njira zotsatirazi zaperekedwa kuti zitithandize kugwiritsira ntchito mogwira mtima zofalitsa zathu zabwino kwambiri zimenezi.

3 Kufunafuna Anthu: M’madera amene anthu ambiri samapezeka panyumba pamene tipita kunyumba ndi nyumba, kufunafuna ndi kulankhula ndi anthu kulikonse kumene apezeka kwakhala kopindulitsa. Mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa September 1996 inatilimbikitsa kulalikira uthenga wabwino kulikonse—m’khwalala, pazoyendera za onse, ndi m’mapaki, poimika galimoto, ndi pamalo a malonda. Inatidziŵitsanso kuti tifunika kupeza njira zolalikirira mwamwaŵi. Kungochitira chitsanzo zimenezi, mlongo wina mpainiya anapita kosungira nyama natenga makope ake a Galamukani! ya August 8, 1996, yokhala ndi nkhani zakuti “Nyama Zokhala Pangozi.” Paola limodzi lokha, anagaŵira makope 40 kwa anthu amene amakonda kwambiri zinyama! Nanga inuyo mwakhalapo ndi chipambano chotani pakulalikira uthenga wabwino kulikonse? Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! limodzinso ndi brosha la Mulungu Amafunanji ndizo kwenikweni zimayenerera umboni wamtundu uliwonse chifukwa zimakhala ndi nkhani zimene zimakhudza moyo wa anthu ndi kuwasonkhezera kuganiza.

4 Kuyambitsa Makambitsirano: Tsamba lakumbuyo la Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996 limalongosola mwatsatanetsatane mmene mungadzikonzere ulaliki wanuwanu wa magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Njira zofananazo zidzagwira bwino ntchito pokonzekera ulaliki wanu wa brosha la Mulungu Amafunanji. Munganene mawu angapo okha kapena mawu ambiri moti nkuphatikizapo lingaliro la m’Malemba. Nkofunika kusankha mosamala mawu oyamba, popeza ndiwo angachititse munthu amene mwamfikirayo kuti mwina apitirize kumvetsera. Ena apeza chipambano ndi mawu oyamba awa: “Ndaŵerenga nkhani ina imene yandilimbikitsa, ndipo ndifuna ndikusonyezeni.” Kapena mungadzutse funso lina lochititsa chidwi limene lidzaloŵetsa winayo m’makambitsirano.

5 Ngati nkoyenera m’dera lanu, mungayese kufunsa mafunso onga otsatirawa mu ulaliki wanu mwezi uno:

◼ “Lerolino timaona zolembalemba pamakoma, zinyatsi, ndi kuipitsa paliponse. Kodi padzafunika chiyani kuti dziko liyere ndi kukhala malo abwino okhalamo?” Yembekezerani yankho, kenako fotokozani kuti muli ndi chidziŵitso chotitsimikiza chonena za pamene dziko lonse lapansi lidzakhala munda wokhawokha ndi mmene zidzachitikira. Sonyezani mawu enieni, lemba lachidule, ndi chithunzi chokongola m’magazini yatsopano, ndiyeno igaŵireni kwa munthuyo pachopereka cha K2.00. Musanamalize makambitsirano anu, yesani kulinganiza kuti mudzapitirize nthaŵi ina.

◼ “Kodi muganiza kuti Mulungu anafuna kuti anthufe tizingidwe ndi mavuto monga amene tili nawo lerolino?” Munthuyo atayankha, munganene kuti: “Muyenera kuti mukulidziŵa pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera, kupempha Ufumu wa Mulungu kudza. Kodi munayamba mwaganizapo kuti Ufumu wa Mulungu nchiyani kwenikweni?” Pitani paphunziro 6 m’brosha la Mulungu Amafunanji, ndipo ŵerengani mafunso ofunsidwa pachiyambi pa phunzirolo. Ndiyeno, poŵerenga ndime 1, sonyezani yankho la funso loyamba. Fotokozani kuti mafunso enawo nawonso ayankhidwa momveka. Gaŵirani broshalo pachopereka cha K3.60, ndiyeno pemphani kuti mudzakumanenso kudzagaŵana chidziŵitso china chonena za Ufumu.

◼ “Anthu ambiri anzeru ayamba kuona kuti zipembedzo za dzikoli ndizo zikuchititsa mavuto a munthu m’malo mowathetsa. Nanga inuyo mukutipo bwanji pamenepa?” Mutamvetsera lingaliro la munthuyo, sonyezani kenakake m’magazini atsopano alionse komwe kangamchititse chidwi ponena za kulephera kwa chipembedzo chonyenga kapena kuyandikira kwa chiwonongeko chake. Mfunseni ngati angakonde kuiŵerenga. Uzanani maina, ndipo pemphani kudzaonananso kuti mudzafotokoze mmene chipembedzo choona sichinawagwiritsire mwala anthu. Ngati nkoyenera, fotokozani mmene munthu wokondweretsedwayo angapezere kope lake.

◼ “Pokhala ndi mavuto onsewa m’mabanja lerolino, kodi munayamba mwadzifunsapo chimene chili chinsinsi chopezera chimwemwe cha banja?” Yembekezerani yankho, ndipo fotokozani kuti m’Baibulo, Mulungu amavumbula chinsinsi chenicheni cha chimwemwe cha banja. Mwinamwake mungaŵerenge Yesaya 48:17. Ndiyeno pitani paphunziro 8 m’brosha la Mulungu Amafunanji, ndipo sonyezani ena a mavesi a Baibulo osagwidwa mawu amene amapereka chitsogozo chodalirika kwa aliyense wa m’banja. Ŵerengani mpambo wa mafunso pachiyambi pa phunzirolo. Funsani ngati munthuyo angakonde kuŵerenga mayankho ake. Ngati akulifuna, mpatseni broshalo pachopereka chamasiku onse. Pemphani kubweranso nthaŵi ina kudzagaŵana naye zitsogozo zinanso zothandiza zimene Baibulo lili nazo pamoyo wa banja wachimwemwe.

6 Mphatika ya m’kope lino la Utumiki Wathu Waufumu inatilimbikitsa kulimbika mtima kuti tipange maulendo obwereza. Inanena kuti kuli bwino kugwiritsira ntchito brosha latsopano kuyambitsira maphunziro a Baibulo paulendo wobwereza ngati sitinayambe paulendo woyamba. Chimene anthu akufunika kwambiri ndicho kuphunzira zimene Mulungu amafuna ndiyeno kuzichita. (Akol. 1:9, 10) Tidzapindulitsadi ena mu April ndi May ngati tingayambe kuwaphunzitsa zimene timadziŵa pazimene Yehova amafuna kuti iwo akhale ndi moyo.—1 Akor. 9:23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena