Changu Chimene Chimautsa Ochuluka
Mtumwi Paulo anayamikira Akorinto chifukwa chakuti changu chawo pantchito yabwino ‘chinautsa [Akristu anzawo] ochuluka’. (2 Akor. 9:2) Kaŵirikaŵiri, munthu m’modzi, banja, gulu la phunziro la buku, kapena mpingo wonse ungachite zofananazo mwachangu chimene ali nacho mu ntchito yolalikira. Nazi njira zina zimene mungasonyezere changu pa utumiki.
◼ Patulani Loŵeruka kukhala Tsiku logaŵira Magazini.
◼ Chitani nawo mbali ina ya Utumiki wakumunda pamasiku a Lamlungu.
◼ Gwiritsani ntchito maola akumadzulo kuchita umboni wamadzulo.
◼ Chitani nawo maulaliki apadera alionse amene akonzedwa.
◼ Gwiritsani ntchito masiku a maholide akuntchito kapena akusukulu kupita muulaliki.
◼ Chirikizani utumiki nthaŵi ya woyendera dera.
◼ Chitani upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena kuposerapo pachaka.
◼ Sinthani zochita zanu kuti muchite upainiya wokhazikika ngati n’kotheka.
Onani 2000 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 17-19.