Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Mar. 15
“Kodi mukuvomereza kuti ulamuliro wolungama ungasandutse dzikoli kukhala malo abwino kwa anthu kukhalamo? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likulonjeza. [Ŵerengani Salmo 37:11.] Tikhoza kusangalala ndi mtendere umenewu, umene udzakhalepo mu ulamuliro wa Mtsogoleri wangwiro amene amutchula mu nkhani izi.”
Galamukani! Apr. 8
“Zivomezi zingaphe anthu ochuluka komanso zingawononge zinthu zambiri zedi. Nthaŵi zambiri anthu opulumuka pangozi zimenezi amakhala opanda nyumba. Amakhala alibiretu zoti n’kuwathandiza kukhalanso ndi moyo wabwino. Galamukani! iyi ikusonyeza zimene anthu okhudzidwa ndi ngozi zoterezi achita kuti apirire mavuto amene amabwera chifukwa cha chivomezi. Ikusonyezanso kuti ulosi wofunika kwambiri m’Baibulo umanena za zivomezi.”
Nsanja ya Olonda Apr. 1
“Ndikufuna ndikuuzeni mawu a m’Baibulo olimbikitsa kwambiri aŵa. [Ŵerengani Mateyu 22:37.] Kodi mukuganiza kuti mawu ameneŵa akutanthauza chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Taonani nkhani iyi yakuti, ‘Funani Mulungu ndi Mtima ndi Maganizo Anu.’ Kodi chikhulupiriro chenicheni n’chofunika kukhudza mtima wokha, kapena ndi maganizo omwe? Yankho lake n’lothandiza kwambiri.”
Galamukani! Apr. 8
“Monga mukudziŵa, masiku ano kusamalira banja si ntchito yamaseŵera, komanso kukhala mayi n’chintchito chovuta. Galamukani! iyi ili ndi malangizo abwino pankhani iyi yamutu wakuti ‘Kodi Kukhala Mayi Kumalira Ukatswiri?’ Ndikusiyirani magazini imeneyi.”