Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/05 tsamba 8
  • Ntchito Yapadera Yogawira Bulosha Latsopano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Yapadera Yogawira Bulosha Latsopano
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 2/05 tsamba 8

Ntchito Yapadera Yogawira Bulosha Latsopano

1 Anthu ambiri masiku ano akuvutika ndi mmene zinthu zilili m’dzikoli, koma ndi ochepa okha amene akudziwa chifukwa chake zinthu zili mmene zililimu, mmene zinthu zidzakhalire m’tsogolo ndiponso zimene angachite kuti adzathe kupulumuka chiweruzo chimene chikubwera. (Ezek. 9:4) Kuti tiwathandize kuzindikira chifukwa chake nthawi yathu ino ili yotere, pakonzedwa ntchito yapadera yogawira bulosha latsopano lakuti Dikirani! Ntchito imeneyi idzachitika kuyambira Lolemba, pa October 18, mpaka Lamlungu, pa November 14.

2 Buloshali tingaligawire pamene tili mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, popanga maulendo obwereza, pochita umboni wa mwamwayi, kapena pamene tili m’malo ena amene mumapezeka anthu ambiri. Komabe, bulosha limeneli la Dikirani! siliyenera kugawidwa mwachisawawa. M’malo mwake, tidzagawira mabuloshawa kwa okhawo amene akufuna kudziwa zimene Baibulo limanena kuti n’chifukwa chiyani m’dzikoli mukuchitika zinthu zimene zikuchitikazi. Kwa amene sanasonyeze chidwi chokwanira pa uthengawu tingathe kuwagawira thirakiti.

3 Mungakope chidwi cha munthu mwa kunena kuti:

◼ “Anthu ambiri akuda nkhawa chifukwa cha mavuto aakulu ndi zochitika zoopsa zimene zafala masiku ano. [Tchulani chitsanzo chodziwika bwino m’dera lanulo.] Kodi mukudziwa kuti zinthu zimenezi zinanenedwa kalekale m’Baibulo? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani lemba logwirizana ndi chitsanzo chimene munatchula chija, monga ngati Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:7, 10, 11; kapena 2 Timoteo 3:1-5.] Baibulo limatiuza chifukwa chake nthawi yathu ino pakuchitika zinthu zotere ndi mmene tsogolo la anthu lidzakhalira. Kodi mukufuna kudziwa zambiri? [Yembekezani ayankhe. Gawirani bulosha ngati waonetsa kuti alidi ndi chidwi.] Sitikulipiritsa kuti munthu apeze buku limeneli. Ngati mukufuna kupereka kangachepe kuti muthandize ntchito ya padziko lonse imeneyi, tiyamikira zopereka zanu.”

4 Kapena njira iyi ingakhale yothandiza kwa inu:

◼ “Anthu ambiri masiku ano akuvutika maganizo ndi zinthu zoopsa zimene zikuchitika m’dzikoli kapena zimene zawachitikira. Ena amadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu salowererapo kuti aletse zinthu zimenezi. Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu adzachotsa zopweteka zonse zimene zikuvutitsa anthu. Taonani zabwino zimene Mulungu adzachitira anthu. [Werengani Salmo 37:10, 11.] Kodi mukufuna kudziwa zambiri?” Pomaliza tchulani zimene tanena kumapeto kwa ndime 3.

5 Yesetsani kulemba dzina ndi adiresi ya munthu aliyense amene wavomera kulandira buloshali, ndipo konzani zobwererako kuti mukakulitse chidwi. Mfundo zosonyeza mmene mungachitire zimenezi zidzaikidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2004. Ngati munthu wasonyeza kuti ali ndi chidwi kwambiri paulendo woyambawo, mukhoza kuyamba naye phunziro la Baibulo nthawi yomweyo pogwiritsa ntchito bulosha la Dikirani! kapena buku lina, monga ngati bulosha la Mulungu Amafunanji.

6 Mudzapeza mabulosha atsopanowa ukatha Msonkhano wa Utumiki umene nkhaniyi iti idzakambidwe. Ndi bwino kuti ofalitsa ndiponso apainiya, poyamba adzatenge mabulosha okhawo amene akuona kuti angakagawire kwa masiku ochepa oyambirira a ntchito yapadera imeneyi. Yehova adalitse ntchito yapadera imeneyi kuti alemekezeke ndi kuti ithandize anthu oona mtima kwina kulikonse.—Sal. 90:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena