Gwiritsani Ntchito Bwino Nthawi Muutumiki
1 Tili ndi ntchito yambiri yoti tichite mu utumiki wathu ndipo nthawi imene yatsala ndi yochepa. (Yoh. 4:35; 1 Akor. 7:29) Komabe titha kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu ya muutumiki mwa kukonzekera ndi kukhala adongosolo.
2 Tizikonzekera: Tisanapite ku msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda, tizionetsetsa kuti tili ndi mabuku omwe tikagwiritse ntchito ndiponso takonzekera kale ulaliki wathu. Msonkhanowo ukangotha ndi pemphero, tizinyamuka mwamsanga kupita m’gawo. Zimenezi zidzachititsa kuti ifeyo ndiponso anzathu amene tikupita nawo m’munda tisawononge nthawi.
3 Ngati ndife amene tikuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda, tizionetsetsa kuti tayamba panthawi yake. Msonkhanowu ukhale wachidule, wamphindi pakati pa 10 ndi 15. Anthu asananyamuke, tionetsetse kuti aliyense akudziwa amene ayende naye ndiponso gawo loti apite.
4 Muutumiki: Msonkhano wokonzekera utumiki ukangotha, tisachedwe kulowa m’gawo popanda chifukwa chenicheni. Ngati tikuona kuti tichoka m’gawo mofulumira, tionetsetse kuti zimenezo zisakachititse ena kuchokanso mofulumira. Tikamayenda ndi gulu, tiziganizira anzathu amene akutidikira kuti timalize kulankhula ndi munthu. Mwina tingafunikire kumusiya mochenjera munthu amene akungofuna kutsutsana nafe kapena tingakonze zodzapitanso kwa munthu amene wasonyeza chidwi.—Mat. 10:11.
5 Popita ku maulendo obwereza, tingapewe kumangoyendayenda mwa kuyamba ndi gawo limodzi kaye tisanapite lina. Tingachitenso bwino kuimbira foni anthu ena kuti tidziwiretu ngati tingakawapeze kunyumba. (Miy. 21:5) Ngati tikuona kuti tichedwa ku ulendo wina wobwereza, tiyenera kukonza zoti gulu limene tikuyenda nalo lizilalikira chapafupi kapena tingakonze zodzabweranso ulendo wina.
6 Tikukhala m’nthawi ya ntchito yaikulu yokolola mwauzimu. (Mat. 9:37, 38) Posachedwapa ntchitoyi itha. Choncho, tiyeni tikhale ndi mtima wofuna kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu muutumiki.