Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira January 14
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Pogwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, sonyezani zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya January. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.15: “Gwiritsani Ntchito Bwino Nthawi Muutumiki.”a Funsani mafunso m’bale wachitsanzo chabwino potsogolera anthu muutumiki wakumunda. Kodi n’chiyani chimene amachita kuti akonzekere kulowetsa anthu m’munda ndi kugwiritsa ntchito bwino nthawi ya utumiki wakumunda?
Mph.20: “Nthawi Zonse Mawu Anu Azikhala . . . Okoleretsa ndi Mchere.”b Pokambirana ndime 2, werengani Yohane 4:7-15, 39.
Mlungu Woyambira January 21
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Tchulani mabuku ogawira mu February, ndipo sonyezani chitsanzo chimodzi. Limbikitsani onse kukawerenga nkhani yakuti “Kumvera Lamulo la Mulungu Losala Magazi” mu mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2005 pokonzekera nkhani ya mu Msonkhano wa Utumiki wa mlungu woyambira February 4.
Mph.10: Kodi Mukugwiritsa Ntchito Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku? Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera yochokera pa mawu oyamba a m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2008. Kambiranani ubwino wokhala ndi nthawi yowerenga Lemba la tsiku ndi ndemanga yake tsiku lililonse. Pemphani omvetsera kuti afotokoze za nthawi imene amachita lemba latsiku ndi phindu limene apeza. Mungakonzeretu ndemanga imodzi kapena ziwiri. Fotokozani mwachidule lemba la chaka cha 2008.
Mph.25: “Chitirani Umboni Bwino Lomwe za Uthenga Wabwino.”c (Ndime 1-10) Yoti ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Funsani mafunso wofalitsa mmodzi kapena awiri amene anachita upainiya wothandiza chaka chatha ngakhale kuti anali ndi zochita zambiri kapena thanzi lofooka. Kodi anakwanitsa bwanji kuchita upainiya? Kodi anapeza chimwemwe chotani? Pokambirana ndime 7, tchulani za ndandanda yokonzekera utumiki wakumunda ya March, April ndi May.
Mlungu Woyambira January 28
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a mwezi wa January. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Kambiranani ndi omvetsera za mu Nsanja ya Olonda ya February 1 ndi Galamukani! ya February. Pambuyo pofotokoza mwachidule za m’magazini iliyonse, pemphani omvetsera atchule nkhani zimene zingakhale zogwira mtima m’gawo lanu ndipo apereke zifukwa chake. Apempheni kuti atchule mfundo zimene zili m’nkhani zimene akufuna kukagwiritsa ntchito pogawira magazini iliyonse. Kodi angafunse mafunso otani kuti ayambitse makambirano? Kodi ndi lemba liti m’nkhaniyo limene akawerenge? Kodi lembalo lingagwirizanitsidwe bwanji ndi nkhaniyo? Pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili pa tsamba 8 sonyezani mmene tingagawirire magazini iliyonse.
Mph.20: “Chitirani Umboni Bwino Lomwe za Uthenga Wabwino.”d (Ndime 11-17) Pokambirana ndime 14, gawirani omvetsera timapepala tapadera toitanira anthu ku Chikumbutso ngati tilipo ndipo fotokozani zimene mpingo wanu wakonza za mmene mungatigawirire m’gawo lanu.
Mph.15: “Thandizani Ophunzira Baibulo Kukhala Ofalitsa Uthenga Wabwino wa Ufumu.”e Ngati nthawi ingalole, pemphani omvetsera kuti afotokoze malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira February 4
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani Bokosi la Mafunso.
Mph.10: Zosowa za pampingo.
Mph.25: “Kodi Mumanyalanyaza?” Yoti ikambidwe ndi mkulu. Musachedwe kuyamba kukambirana ndi omvetsera nkhani yakuti “Kumvera Lamulo la Mulungu Losala Magazi” mu mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2005 ndime 5 mpaka 14. Malizani ndi kuwerenga ndime yomaliza ndipo limbikitsani onse kuwerenga mofatsa nkhani zimene zatchulidwa zochokera mu Nsanja ya Olonda ndi Utumiki Wathu wa Ufumu. Fotokozani mmene aliyense amene sanalembebe khadi lake la DPA angagwiritsirire ntchito mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006 popanga chosankha chokhudza tizigawo ta magazi ndi chithandizo chamankhwala n’kulemba zimene wasankhazo pa khadi la DPA. Ena amene analemba kale khadi lawo la DPA, ngati angachite bwino kuonanso zimene anasankha ndipo ngati angafune kusintha mfundo zina angalembenso khadi latsopano.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.