Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda June 1
“Anthu ena amakhulupirira nyenyezi kuti adziwe za mtsogolo. Kodi mukuganiza kuti nyenyezi zingakuthandizeni? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Baibulo limanena pa nkhani yokhulupirira zinthu zakuthambo pofuna kudziwa za mtsogolo. [Werengani Deuteronomo 18:10-12.] Nkhaniyi ikufotokoza mfundo zinanso zimene Baibulo limanena pa nkhani yokhulupirira nyenyezi.” Musonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 18.
Galamukani! June
“Matchalitchi ambiri amalipiritsa ngati anthu akufuna kubatizidwa, kuchita ukwati komanso mwambo wamaliro. Kodi mukuganiza kuti zimenezi n’zoyenera? [Yembekezani ayankhe.] Taonani malangizo amene Yesu anapatsa ophunzira ake. [Werengani Mateyo 10:7, 8b.] Nkhani ino ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani yolipiritsa munthu akafuna kuchita mwambo winawake kutchalitchi.” Muonetseni nkhani imene yayambira patsamba 22.
Nsanja ya Olonda July 1
“Anthu ambiri akafuna kutchula Mulungu amangoti Ambuye. Kodi mukudziwa kuti Baibulo limatiuza dzina lenileni la Mulungu? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yesaya 42:8a.] Magaziniyi ikufotokoza chifukwa chake dzina la Mulungu linachotsedwa m’mabaibulo ena. Komanso ikufotokoza zimene kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauza.”
Galamukani! July
“Anthu ambiri padziko lonse akuda nkhawa chifukwa cha mavuto a zachuma. Amene anachotsedwa ntchito ali ndi nkhawa komanso amene ali pa ntchito amada nkhawa kuti mwina tsiku lina ntchito yawo idzatha. Kodi mukuganiza kuti mawu awa angatithandize kuti tisamade nkhawa? [Werengani Mateyo 6:34. Kenako yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ili ndi mfundo zothandiza zokhudza zimene tingachite kuti tisamawononge ndalama komanso kuti tisamade nkhawa.”