Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda August 1
“Kodi mukuganiza kuti anthu amafunikira chiyani kuti akhale osangalala? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Mateyo 5:3.] Apa tangowerenga mfundo imodzi yokha imene Yesu anafotokoza pa nkhani yokhala wosangalala. Nkhaniyi ikufotokoza zimene Yesu anaphunzitsa zimene zingatithandize kukhala osangalala.” Sonyezani nkhani imene ikuyambira patsamba 16.
Galamukani! August
“Mafilimu ambiri masiku ano amaonetsa zinthu zokhudzana ndi ziwanda, zamatsenga ndi zaufiti. Kodi mukuganiza kuti ziwanda zilipodi? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani 1 Akorinto 10:20.] Nkhani iyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena zokhudza ziwanda komanso mmene tingadzitetezere ku ziwanda.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 20.
Nsanja ya Olonda September 1
Tchulani nkhani imene yangochitika kumene kwanuko. Kenako muwafunse kuti: “Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani anthu amachita zinthu zoipa ngati zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Koma Baibulo limatipatsa chiyembekezo chakuti zoipa zidzatha. [Werengani 2 Petulo 3:13.] Magazini ino ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza zimene zinayambitsa kuti zinthu zoipa zizichitika, ndi mmene Mulungu adzathetsere zoipa zonse.”
Galamukani! September
“Kodi mukuganiza kuti mafoni am’manja, mauthenga a pakompyuta, Intaneti ndi njira zina zamakono zolankhulirana zathandiza kuti anthu asamasungulumwe, kapena zangowonjezera vutoli? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chinthu chimodzi chimene chingatithandize kuti tisamasungulumwe kwambiri. [Werengani Machitidwe 20:35.] Magaziniyi ili ndi malangizo enanso ochokera m’Baibulo othandiza kuti munthu asamasungulumwe kwambiri.”