Njira Ina Imene Tingagwiritsire Ntchito Kabuku ka Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?
M’magawo amene timalalikira, anthu ambiri amene sali m’zipembedzo zachikhristu, Baibulo salidziwa bwinobwino. Ofalitsa ena akamaphunzira ndi anthu oterewa buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? amagwiritsanso ntchito kabuku ka Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? kuti awathandize kudziwa mwachidule zimene zili m’Baibulo. Mwachitsanzo, m’bale wina amasonyeza wophunzira mutu 1 wa kabukuka akamaphunzira mutu 3 wa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ndiyeno nthawi iliyonse akamaliza kuphunzira amakambirana mutu wina wa m’kabukuka. Kodi inuyo mukuphunzira ndi munthu wina amene sadziwa zambiri za Baibulo? Kuti muthandize munthu wotereyu kuphunzira ‘malemba oyera amene angathe kumupatsa nzeru zomuthandiza kuti adzapulumuke,’ konzani zoti mukamaphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni muziphunziranso kabuku ka Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?—2 Tim. 3:15.