Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/12 tsamba 2
  • “Zimene Munganene Pogawira Magazini mu . . .”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Zimene Munganene Pogawira Magazini mu . . .”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Magazini Amalengeza Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Magaziniwo Mumawaŵerenga?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 12/12 tsamba 2

“Zimene Munganene Pogawira Magazini mu . . .”

Mwezi uliwonse pa Msonkhano wa Utumiki timakhala ndi nkhani yonena za mmene tingagawirire magazini. Cholinga cha nkhaniyi si kukambirana nkhani zimene zili m’magaziniwa. M’malomwake, cholinga chake n’kukambirana mmene tingagawirire magaziniwa. Chotero m’bale amene akukamba nkhaniyi amalangizidwa kuti anene mawu oyamba achidule kwambiri amene angathandize abale ndi alongo kukhala ndi chidwi pa magaziniwa. Kenako amapempha abale ndi alongo kuti afotokoze zimene anganene pogawira magaziniwa pogwiritsa ntchito nkhani imodzi ndi imodzi kapena nkhani zoyambirira zingapo. Zimenezi zimathandiza kuti abale ndi alongo onse athe kutsatira komanso kupeza njira zimene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. M’malo mopempha omvera kuti afotokoze zonse zimene anganene pogawira magaziniwo, m’bale amene akukamba nkhaniyi amapempha ofalitsa kuti anene funso limene lingachititse chidwi anthu a m’gawolo komanso lemba limene wofalitsayo angawerenge. Iye amamaliza nkhaniyi ndi zitsanzo zosonyeza mmene tingagawirire magazini iliyonse. Tonsefe tikulimbikitsidwa kuti tizikonzekereratu kuti tizikapereka ndemanga. Ngati tonse titamakonzekera, nkhaniyi ingathandize kuti tizilimbikitsana.—Miy. 27:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena